2 Timothy 3:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena mwa iwo amaloŵa m'nyumba za anthu nkumakanyenga akazi ofooka, olemedwa ndi katundu wa machimo. Akazi ameneŵa amatengeka ndi zilakolako zamitundumitundu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundu mitundu: