2 Timothy 3:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe Yane ndi Yambere adaaukira Mose, anthu amenewonso amaukira choona. Nzeru zao nzobuntha, ndipo pa za chikhulupiriro ndi anthu olephera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo monga momwe Yane ndi Yambre anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana naco coonadi; ndiwo anthu obvunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pacikhulupiriro.