2 Timothy 4:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ndinkadziteteza pa mlandu wanga poyamba paja, panalibe ndi mmodzi yemwe amene adabwera kudzandithandiza, onse adangondisiya ndekha. Mulungu aŵakhululukire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Podziteteza koyamba pa mlandu wanga, panalibe ndi mmodzi yemwe amene anandithandiza, koma aliyense anandithawa. Mulungu awakhululukire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa codzikanira canga coyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; cimeneco cisawerengedwe cowatsutsa.