2 Timothy 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse aŵamve. Motero ndidapulumuka m'kamwa mwa mkango.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ambuye anayima nane limodzi, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, uthenga ulalikidwe kwambiri, ndikuti anthu a mitundu ina amve. Ndipo ndinalanditsidwa mʼkamwa mwa mkango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine cilalikiro cimveke konse konse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.