2 Timothy 4:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: