2 Timothy 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja ine ndiye moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthaŵi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m'moyo uno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndirimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.