3 John 1:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndikabwera, ndidzakumbutsa ntchito zimene amachita. Iye amandilalatira ndi mau oipa. Ndipo sachita zokhazi ai, komanso iyeiyeyo amakana kulandira abale, ndipo anthu ofuna kuŵalandira, iye amaŵaletsa, nkumaŵatulutsa mu mpingo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ndikabwera ndidzakumbutsa zimene iye amachita. Iye amafalitsa nkhani zabodza zonena ife. Ndipo sakhutira ndi zimenezo, komanso iyeyo amakana kulandira abale. Komanso amaletsa amene akufuna kutero, ndipo amawachotsa mu mpingo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa nchito zace zimene aeitazi, zakunena zopanda pace pa ife ndi mau oipa; ndipopopeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powaturutsa mu Mpingo,