3 John 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Demetrio anthu onse amamchitira umboni wabwino. Ngakhale choona chomwe chimamchitira umboni. Ifenso tikumchitira umboni, ndipo iweyo ukudziŵa kuti umboni wathu ndi woona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense akumuchitira umboni wabwino wa Demetriyo. Ngakhale choona chomwe chimamuchitira umboni, ndipo iweyo ukudziwa kuti umboni wathu ndi woona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Demetriyo, adamcitira umboni anthu onse, ndi coonadi comwe; ndipo ifenso ticita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.