Acts 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataloŵa mumzindamo, adakwera ku chipinda cham'mwamba kumene ankakhala: panali Petro, Yohane, Yakobe ndi Andrea; Filipo ndi Tomasi; Bartolomeo ndi Mateyo; Yakobe (mwana wa Alifeyo,) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,) ndiponso Yudasi (mwana wa Yakobe.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adalowa, anakwera ku cipinda ca pamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyu, ndi Simoni Zelote, ndi Yuda mwana wa Yakobo.