Acts 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja m'buku la Masalimo muli mau akuti, “ ‘Nyumba yake isanduke bwinja, pasakhale munthu wogonamo.’ Muli mau enanso akuti, “ ‘Wina alandire ntchito yake.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang'aniro wake autenge wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro anati, “Pakuti kwalembedwa mʼbuku la Masalimo kuti, “Nyumba yake isanduke bwinja, ndipo pasakhale wogonamo. Ndiponso, “Wina atenge ntchito yake yautsogoleri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo, Pogonera pace pakhale bwinja, Ndipo pasakhale munthu wogonapo; Ndipo uyang'aniro wace autenge wina.