Acts 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zace, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumuwa Mulungu;