Acts 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Petro adayamba kusinkhasinkha za tanthauzo la zimene adaaziwona m'masomphenya zija. Nthaŵi yomweyo anthu amene Kornelio adaaŵatuma aja, ankafunsa za nyumba ya Simoni, ndipo tsopano adaadzaima pa khomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pokayika-kayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti ciani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Komeliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pa cipata,