Acts 10:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adati, “Kornelio, mkulu wa gulu la asilikali 100, watituma. Iyeyo ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu, ndipo Ayuda onse amamtama. Mngelo wa Mulungu adamuuza kuti akuitaneni kuti mupite kunyumba kwake akamve mau amene muli nawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Komeliyo kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umcitira umboni, anacenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke ku nyumba yace, ndi kummvetsa mau anu.