Acts 10:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Petro adaŵaloŵetsa m'nyumba, naŵasamala. M'maŵa mwake adanyamuka napita nawo, ndipo abale ena a ku Yopa adamperekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anawalowetsa nawachereza. Ndipo m'mawa mwake ananyamuka natuluka nao, ndi ena a abale a ku Yopa anamperekeza iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anawalowetsa nawacereza. Ndipo m'mawa mwace ananyamuka naturuka nao, ndi ena a abale a ku Yopaanamperekezaiye.