Acts 10:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake adafika ku Kesareya. Kornelio ankaŵadikira, atasonkhanitsa abale ndi abwenzi ake apamtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake analowa m'Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace analowa m'Kaisareya, Koma Komeliyo analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ace ndi mabwenzi ace eni eni.