Acts 10:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Petro adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa kuti Myuda saloledwa konse kuyanjana ndi munthu wa mtundu wina, ngakhale kuloŵa m'nyumba mwake. Koma Mulungu wandidziŵitsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ngwosayera kapena wonyansa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa;