Acts 10:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Komeliyo anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lacisanu ndi cinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wobvala cobvala conyezimira,