Acts 10:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, 1 ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.