Acts 11:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Okhulupirira Khristu aja, amene anali atabalalikana chifukwa cha mazunzo omwe adabuka pa nkhani ija ya Stefano, adafika mpaka ku Fenisiya, ku Kipro, ndiponso ku Antiokeya. Sankalalika mau kwa munthu wina aliyense, koma kwa Ayuda okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano amene anabalalika chifukwa cha mazunzo amene anayamba ataphedwa Stefano, anapita mpaka ku Foinike, ku Kupro ndi ku Antiokeya, ndipo ankalalikira kwa Ayuda okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo iwotu, akubalalika cifukwa ca cisautsoco cidadza pa Stefano, anafikira ku Foinike, ndi Kupro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha.