Acts 11:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmodzi mwa iwo, dzina lake Agabu, adaimirira, ndipo ndi mphamvu za Mzimu Woyera adalosa kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lapansi. Njalayo idabweradi pa nthaŵi ya Klaudio.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyanamuka mmodzi wa iwo, dzina lace Agabo, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudiyo.