Acts 11:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine ndinkapemphera m'mudzi wa Yopa. Ndidaachita ngati kukomoka, ndiye ndidaona ngati kutulo chinthu china chikutsika pansi kuchokera kumwamba. Chinkaoneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai, ndipo chidafika pamene panali ineyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndimapemphera mu mzinda wa Yopa ndipo ndili ngati wokomoka ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chokhala ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa msonga zake zinayi, ndipo chinatsikira pa ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine;