Acts 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiŵiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata choloŵera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumudzi; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi paciwiri, anadza ku citseko cacitsulo cakuyang'ana kumudzi; cimene cidawatsegukira cokha; ndipo anaturuka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamcokera.