Acts 12:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Petro adadzidzimuka nati, “Tsopano ndikudziŵadi kuti Ambuye anatuma mngelo wao ndipo andipulumutsa kwa Herode, ndi ku zoipa zonse zimene Ayuda ankayembekeza kuti zidzandichitikira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wace nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku cilingiriro conse ca anthu a Israyeli.