Acts 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atazindikira liwu lake kuti ndi la Petro, adakondwa kwambiri, kotero kuti sadatsekule chitsekocho, koma adathamangiranso m'kati nakawuza ena aja kuti, “Petro ali pakhomopa!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pozindikira mau ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, “Petro ali pa khomopa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pozindikira mau ace a Petro, cifukwa ca kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.