Acts 12:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Petro adakweza dzanja kuti iwo akhale chete, naŵafotokozera m'mene Ambuye adaamtulutsira m'ndende muja. Ndipo adati, “Mumuuze Yakobe ndi abale ena aja zimenezi.” Pamenepo iye adatuluka napita kwina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro anakweza dzanja ndi kuwawuza kuti akhale chete ndipo anawafotokozera mmene Ambuye anamutulutsira mʼndende. Iye anati, “Uzani Yakobo ndi abale ena za zimenezi.” Kenaka anachoka napita kumalo ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale cete, anawafotokozera umo, adamturutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi, Ndipo anaturuka napita kwina.