Acts 12:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Herode adaaŵakwiyira anthu a ku Tiro ndi a ku Sidoni. Tsono anthuwo adadza pamodzi kwa iye. Adaayamba akopa Blasito, kapitao wa ku nyumba ya mfumu kenaka nkukapempha mtendere, chifukwa chakudya cha m'dziko laolo chinkachokera m'dziko la mfumuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Herode anakwiyira anthu a ku Turo ndi Sidoni; anthuwo anagwirizana zoti akambirane naye. Atapeza thandizo kuchokera kwa Blasito, wantchito wokhulupirika wa mfumu, anapempha kuti pakhale mtendere, chifukwa dziko lawo limadalira dziko la mfumuyo pa chakudya chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Herode anaipidwa nao a ku Turo ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zocokera ku dziko la mfumu.