Acts 12:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anai anai, amdikire iye; ndipo anafuna kumturutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.