Acts 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwadzidzidzi kudafika mngelo wa Ambuye ndipo kuŵala koti mbee kudaunika m'chipindamo. Mngeloyo adagunduza Petro m'nthitimu kuti amdzutse, ndipo adati, “Dzuka msanga!” Pompo maunyolo aja adakolopoka m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga, Ndipo maunyolo anagwa kucoka m'manja mwace.