Acts 12:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Petro adatuluka namtsata, osazindikira kuti zimene mngelo ankachitazo nzoona. Ankangoyesa kuti akuwona zinthu m'masomphenya chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti ncoona cocitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.