Acts 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ona dzanja la Ambuye likukantha tsopano apa. Ukhala wakhungu osaonanso dzuŵa pa kanthaŵi.” Nthaŵi yomweyo khungu ndi mdima zidamgweradi, ndipo adayamba kufunafuna anthu oti amgwire dzanja ndi kumtsogolera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye liri pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapeoya dzuwa nthawi, Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamoka oaf una wina womgwira dzanja.