Acts 13:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene atamcotsa iye, anawautsira Davine akhale mfumu yao; amenenso anamcitira umboni, nati, Ndapeza Davine, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzacita cifuniro canga conse.