Acts 13:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yohane amatsiriza ntchito yake anati: ‘Mukuganiza kuti ine ndine yani? Ine sindine ameneyo ayi, koma Iye akubwera pambuyo panga, amene ine sindine woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakukwaniritsa njira yace Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ace.