Acts 13:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Yerusalemu ndi atsogoleri awo sanazindikire Yesu, komabe pomuweruza Yesu anakwaniritsa mawu a Aneneri amene amawerengedwa Sabata lililonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.