Acts 13:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu osonkhana aja atamwazikana, Ayuda ambiri, ndiponso anthu a mitundu ina otembenuka nkumatsata zachiyuda, adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Aŵiriŵa adalankhula ndi anthu aja, naŵapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adaŵachitira mwa kukoma mtima kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m'chisomo cha Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatha mapemphero, Ayuda ambiri ndi anthu odzipereka otembenukira ku Chiyuda anatsatira Paulo ndi Barnaba, iwo anayankhula ndi anthuwo ndipo anawapempha kuti apitirire mʼchisomo cha Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata. Paulo ndi Bamaba; amene, polankhula nao, 8 anawaumiriza akhale m'cisomo ca Ambuye.