Acts 13:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Paulo ndi Barnabasi adalankhula molimbika, adati, “Kudaayenera ndithu kuti tiyambe talalika mau a Mulungu kwa inu. Tsono popeza kuti mwaŵakana, ndipo potero mwaonetsa nokha kuti ndinu osayenera kulandira moyo wosatha, ife tikusiyani, tipita kwa anthu akunja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Paulo ndi Bamaba analimbika mtima ponena, nati, 9 Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. 10 Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.