Acts 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika ku mzinda wa Salami, adalalika mau a Mulungu m'nyumba zamapemphero za Ayuda. Analinso ndi Yohane womaŵathandiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anafika ku Salamisi, analalikira Mawu a Mulungu mʼMasunagoge a Ayuda. Iwo anali ndi Yohane monga wowatumikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.