Acts 13:50 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ayuda aja adautsa mitima ya akazi ena apamwamba opembedza Mulungu, ndiponso ya atsogoleri achimuna amumzindamo. Tsono adayambitsa mazunzo osautsa Paulo ndi Barnabasi, naŵapirikitsa m'dziko mwaomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, 12 nawautsira cizunzo Paulo ndi Bamaba, ndipo ana wapitikitsaiwom'malire ao.