Acts 14:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene zidachitika ku Antiokeya, zidachitikanso ku Ikonio. Paulo ndi Barnabasi adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Adaphunzitsa mwamphamvu, kotero kuti anthu ambirimbiri, Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina, adakhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pa Ikoniyo kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikuru la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira.