Acts 14:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu onse aja adaona zimene Paulo adachita, adafuula m'Chilikaoniya kuti, “Yatitsikira milungu yooneka ngati anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m'chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene makamu anaona cimene anacita Paulo, anakweza mau ao, nati m'cinenero ca Lukaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.