Acts 14:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumba yopembedzeramo Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo. Tsono wansembe wake adabwera ku zipata atatenga ng'ombe yozekedwa maluŵa m'khosi. Iyeyo pamodzi ndi anthu onse aja adaafuna kudzapereka nsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wansembe wa Zeu wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.