Acts 14:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthuni, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napfuula Dati, Anthuni, bwanji mucita zimenezi? ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zacabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo: