Acts 14:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe sankaleka kudzichitira umboni mwa zabwino zimene amachita. Kuchokera kumwamba amakupatsani mvula ndi nyengo za zipatso. Amakupatsani zakudya ndi zina zambiri zodzaza mitima yanu ndi chimwemwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sanadzisiyira Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anacita zabwino, nakupatsani inu zocokera kumwamba mvulaodi nyengoza zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi cakudya ndicikondwero.