Acts 14:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kudabwera Ayuda ena ochokera ku Antiokeya ndi ku Ikonio nakopa anthu aja. Tsono anthuwo adamponya Pauloyo miyala, kenaka nkumuguzira kunja kwa mzinda, chifukwa ankayesa kuti wafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika kumeneko Ayuda kucokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulomiyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.