Acts 14:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adafika kumeneko, adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokozera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo, ndiponso m'mene Iye adaatsekulira anthu a mitundu ina njira kuti akhulupirire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anacita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la cikhulupiriro.