Acts 14:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace anakhala nthawi yaikuru nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anacitira umboni mau a cisomo cace, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zicitidwe ndi manja ao.