Acts 15:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena ochokera ku Yudeya adabwera ku Antiokeya, namaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuumbala potsata mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapandakudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.