Acts 15:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse mumsonkhanomo adangoti chete nkumamvetsera Barnabasi ndi Paulo akufotokoza za m'mene Mulungu adachitira zizindikiro ndi zozizwitsa pakati pa akunja kudzera mwa iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Bamaba ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anacita nao pa amitundu.