Acts 15:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simoni wafotokoza za m'mene Mulungu pachiyambi pomwe adakumbukira anthu a mitundu ina, pa kupatula ena pakati pao kuti akhale anthu akeake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lace.