Acts 15:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Paulo ndi Barnabasi adatsutsana nawo kolimba. Tsono abale adapangana kuti Paulo ndi Barnabasi, ndi abale ena a ku Antiokeya, apite ku Yerusalemu kukakambirana ndi atumwi ndi akulu a mpingo za nkhaniyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Paulo ndi Bamaba anacitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Bamaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akuru kukanena za funsolo.