Acts 15:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti aŵatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo cinakomera atumwi ndi akuru ndi Eklesia yensekusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Bamaba; ndiwo Yuda wochedwa Barsaba, ndi Sila, akuru a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo: